LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • ijwbv nkhani 40
  • Miyambo 16:3—“Peleka Zocita Zako kwa AMBUYE”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Miyambo 16:3—“Peleka Zocita Zako kwa AMBUYE”
  • Kufotokoza Mavesi a m’Baibulo
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Tanthauzo la Miyambo 16:3
  • Nkhani yonse ya pa Miyambo 16:3
  • Miyambo 3:5, 6—“Usamadalile Luso Lako Lomvetsa Zinthu”
    Kufotokoza Mavesi a m’Baibulo
  • Salimo 37:4—“Udzikondweretsenso mwa Yehova”
    Kufotokoza Mavesi a m’Baibulo
  • Miyambo 17:17—“Bwenzi Lenileni Limakukonda Nthawi Zonse”
    Kufotokoza Mavesi a m’Baibulo
  • Mulungu “Akwanilitse Zofuna Zanu”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
Kufotokoza Mavesi a m’Baibulo
ijwbv nkhani 40

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Miyambo 16:3—“Peleka Zocita Zako kwa AMBUYE”

“Zocita zako zonse uzisiye mʼmanja mwa Yehova, ndipo mapulani ako adzayenda bwino.”—Miyambo 16:3, Baibulo la Dziko Latsopano.

“Peleka zocita zako kwa AMBUYE, ndipo zolingalila zako zidzakhazikika.”—Miyambo 16:3, New International Version.

Tanthauzo la Miyambo 16:3

Mwambi uwu umatsimikizila anthu amene amalambila Mulungu woona kuti zinthu zidzawayendela bwino ngati amamudalila mwa kufunafuna malangizo ake ndi kuwatsatila.

“Zocita zako zonse uzisiye mʼmanja mwa Yehova.” Anthu amene amalambila Yehova,a modzicepetsa amamupempha kuti awathandize asanasankhe zocita. (Yakobo 1:5) N’cifukwa ciyani? Cifukwa cimodzi n’cakuti anthufe nthawi zambili sitingathe kulamulila zimene zimacitika pa moyo wathu. (Mlaliki 9:11; Yakobo 4:13-15) Cifukwa cina n’cakuti tingakhale kuti sitikudziwa mocitila zinthu zimene tikufuna kucita. Pa zifukwa zimenezi anthu ambili aona kuti n’canzelu kusiya zocita zawo m’manja mwa Mulungu. Amacita izi mwa kupemphela kwa iye kuti awatsogolele komanso mwa kucita zinthu mogwilizana ndi cifunilo cake comwe cimapezeka m’mawu ake Baibulo.—Miyambo 3:5, 6; 2 Timoteyo 3:16, 17.

Mawu akuti “peleka zocita zako kwa AMBUYE”b kwenikweni amatanthauza “kupeleka nchito zako kwa AMBUYE.” Malinga ndi buku lina, mawuwa amanena za “munthu amene akucotsa katundu pamsana pake ndi kuuika pa munthu wina wamphamvu kuposa iye ndiponso amene angakwanitse kunyamula katunduwo.” Anthu odzicepetsa amene amadalila Mulungu amakhala otsimikiza kuti iye adzawathandiza.—Salimo 37:5; 55:22.

Mawu akuti “zocita zako zonse” satanthauza kuti Mulungu angavomeleze kapena kudalitsa mapulani alionse amene anthu angakhale nawo. Kuti munthu alandile madalitso a Yehova, mapulani ake ayenela kukhala ogwilizana ndi mfundo zake komanso cifunilo cake. (Salimo 127:1; 1 Yohane 5:14) Mulungu samadalitsa anthu osamvela. “Koma amasokoneza mapulani a anthu oipa.” (Salimo 146:9) Panthawi imodzimodzi, iye amathandiza aja amene amaonetsa kuti ndi ogonjela mwa kulemekeza mfundo zake zopezeka m’Baibulo.—Salimo 37:23.

“Ndipo mapulani ako adzayenda bwino.” Mabaibulo ena amamasulila mawuwa kuti “zolingalila zako zidzakhazikika.” M’malemba a Ciheberi, amene anthu ambili amati Cipangano Cakale, mawu amene anawamasulila kuti “kukhazikika” amakamba za kuyala maziko. Ndipo nthawi zambili amakamba za kukhazikika kwa zinthu zimene Mulungu analenga. (Miyambo 3:19; Yeremiya 10:12) Mofananamo, Mulungu adzcititsa kuti mapulani a anthu amene iye amaona kuti akucita zolungama akhazikike. Adzawathandiza kukhala ndi moyo wabwino, wamtendele, komanso wacimwemwe.—Salimo 20:4; Miyambo 12:3.

Nkhani yonse ya pa Miyambo 16:3

Mwambiwu unalembedwa ndi Mfumu Solomo, amene analemba mbali yaikulu ya buku la Miyambo. Solomo anatha kulankhula miyambi masauzande cifukwa ca nzelu zimene Mulungu anamupatsa.—1 Mafumu 4:29, 32; 10:23, 24.

Mu caputala 16, Solomo akuyamba mwa kutamanda Mulungu cifukwa ca nzelu zake ndipo akuonetsa kuti Mulungu amanyansidwa ndi anthu onyada. (Miyambo 16:1-5) Kenako caputalaci cikuonetsa wowelenga mfundo yofunika kwambili imene imapezeka mobwelezabweleza m’buku la Miyambo. Mfundoyi ndi yakuti: Anthu angakhaledi anzelu komanso opambana pokhapo ngati ndi odzicepetsa ndipo amalola kuti Mulungu awatsogolele. (Miyambo 16:3, 6-8, 18-23) Mfundo yoona imeneyi imapezeka nthawi zambili m’Baibulo.—Salimo 1:1-3; Yesaya 26:3; Yeremiya 17:7, 8; 1 Yohane 3:22.

Welengani Miyambo caputala 16 m’Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika. Baibulo losavuta kuwelenga limeneli likupezeka longomvetsela, muli manotsi ofotokozela, malifalensi, zithunzi, mavidiyo ndiponso ma mapu.

Onelelani vidiyo yaifupi iyi imene ifotokoza mfundo za m’buku la Miyambo.

a Yehova ndilo dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova N’ndani?”

b Mawu oyamba m’Baibulo la New International Version Study Bible amanena kuti Baibuloli limagwilitsa nchito mawu akuti “AMBUYE” (olembedwa m’zilembo zazikulu) pamalo pomwe panali dzina lenileni la Mulungu. Kuti mudziwe cifukwa cake izi zingasokoneze owelenga, onani nkhani yakuti, “Yesaya 42:8—‘Ine ndine AMBUYE.’”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani