Mawu Amunsi
a Koran imakamba za kubadwa kwa Yesu kozizwitsa pa Surah 19 (Mariya). Imati: “Tinatumiza mzimu Wathu kwa [Mariya] wooneka ngati munthu wamkulu. Ndipo pamene iye anauona anati: ‘Wacifundoyo andichinjilize kwa inu! Ngati mumaopa Ambuye, mundisiye ndi kupitiliza ulendo wanu.’ Koma mzimu unayankha kuti: ‘Ndine mthenga wa Ambuye wako, ndipo ndabwela kukupatsa mwana woyela.’ Iye anayankha kuti: ‘Ndingabale bwanji mwana ine namwali wosadziŵa mwamuna?’ Poyankha mzimu unati: ‘Ndi cifunilo ca Ambuye. Izi si zovuta kwa Iye. Ambuye ati: “Mwana ameneyo adzakhala cizindikilo kwa anthu onse ndi dalitso locokela kwa Ife. Uthenga Wathu ndi umeneo.”’”