Mawu Amunsi
d Malinga ndi pangano la Cilamulo, mkazi amene wabeleka mwana anali kufunika kupeleka nsembe ya macimo kwa Mulungu. (Levitiko 12:1-8) Zimenezi zinali kukumbutsa Aisiraeli kuti makolo amapatsila ana ao ucimo. Ndipo lamulo limeneli linawathandiza kuona kubadwa kwa mwana moyenelela ndi kuwathandiza kuti asamatsatile miyambo yacikunja yokondwelela tsiku la kubadwa.—Salimo 51:5.