Mawu Amunsi
c Cinthu cina cimene cinapangitsa kuti Ophunzila Baibulo ena aone macenjezowo mopepuka cinali cakuti macenjezowo anali kupelekedwa makamaka kwa a 144,000, amene ndi kagulu ka nkhosa ka Kristu. M’Nkhani 5 tidzaona kuti caka ca 1935 cisanafike, Ophunzila Baibulo anali kukhulupilila kuti “khamu lalikulu,” monga mmene lafotokozedwela pa Chivumbulutso 7:9, 10, lidzaphatikizapo mamembala ambilimbili a machalichi acikristu. Anali kukhulupililanso kuti anthu amenewa adzakhala m’gulu laciŵili la anthu amene adzapita kumwamba cifukwa cocilikiza Kristu m’nthawi yamapeto.