Mawu Amunsi
d Mu September caka ca 1920, magazini ya The Golden Age (imene tsopano ndi Galamukani!) inafotokoza zizunzo zambili zimene abale anakumana nazo panthawi ya nkhondo ku England, Germany ndi ku United States ndipo zina zinali zankhanza kwambili. Komabe, kwa zaka zambili nkhondo ya padziko lonse isanacitike, zinzunzo sizinali kucitika kaŵilikaŵili.