Mawu Amunsi
b Nthawi imeneyi ingaoneke yaitali kwambili masiku ano. Koma tiyenela kukumbukila kuti kale anthu anali kukhala ndi moyo nthawi yaitali kwambili. Mwacitsanzo, panali anthu anai amene moyo wao unalowelana kucokela nthawi ya Adamu kufika nthawi ya Abulahamu. Adamu anakhalabe ndi moyo mpaka pamene Lameki, atate wake wa Nowa anabadwa. Lameki anakhalabe ndi moyo mpaka pamene Semu, mwana wa Nowa anabadwa. Semu anakhalabe ndi moyo mpaka pamene Abulahamu anabadwa.—Gen. 5:5, 31; 9:29; 11:10, 11; 25:7.