Mawu Amunsi
c Dzina lakuti “Satana” limapezeka nthawi zokwana 18 m’Malemba a Ciheberi. Koma dzina limeneli limapezeka nthawi zokwana 30 m’Malemba a Cigiriki Acikristu. Malemba a Ciheberi sanafotokoze kwambili za Satana, koma anafotokoza kwambili zokhudza Mesiya. Pamene Mesiya anabwela, iye anathandiza anthu kumudziŵa bwino Satana, ndipo Malemba Acigiliki Acikristu amafotokoza bwino zimenezi.