Mawu Amunsi
a N’kwanzelu kunena kuti cionongeko ca “Babulo Wamkulu” cikuimila cionongeko ca magulu onse a zipembedzo osati kuphedwa kwa anthu onse a m’zipembedzo zimenezo. Motelo, anthu ambili a m’zipembedzo zimenezi, sadzaphedwa pamene Babulo adzaonongedwa. Zikadzatelo, io adzayesa kupewa kugwilizana ndi cipembedzo poyela, mogwilizana ndi mau a pa Zekariya 13:4-6.