Mawu Amunsi
a Katswili wina wa ku German wochedwa Heinrich Meyer anati: “Poona . . . kuti thupi la Yesu linali lathunthu (kutanthauza kuti anali wamoyo), ndipo magazi ake anali asanakhetsedwe, palibe aliyense [atumwi] amene akananena . . . kuti akudyadi thupi leni-leni kapena kumwa magazi eni-eni a Ambuye. Ndipo Yesu sakanafuna kuti mau akewo amvedwe mwa njila yolakwika imeneyo cifukwa anali kudziwa kuti ophunzila ake sakanavomeleza zimenezo.”