Mawu Amunsi
b Kale anthu a ku Iguputo anali kudya makeke ndi mikate ya mitundu yosiyanasiyana yoposa 90. Conco, mkulu wa atumiki a Farao ophika mikate anali ndi udindo wapamwamba. Komanso mkulu wa opeleka cikho anali kuyang’anila atumiki a Farao amene anali kuonetsetsa kuti vinyo wopita kwa Farao unali wokoma ndiponso wosaipitsidwa ndi mankhwala amene angaphe mfumu. Panthawiyo, vuto la kupha mafumu kapena kuwacitila ciwembu linali lofala. Motelo, nthawi zambili wopelekela cikho anali kukhalanso mlangizi wodalilika wa mfumu.