Mawu Amunsi
a Pamene Yesu anali kukamba zimene zidzaonetsa kuti tili m’masiku otsiliza, anafotokozela ophunzila ake mafanizo angapo. Coyamba, anakamba za “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” kagulu kang’ono ka abale odzozedwa amene anali kudzatsogolela anthu a Mulungu. (Mat. 24:45-47) Ndiyeno, anapeleka mafanizo okamba za odzozedwa onse. (Mat. 25:1-30) Potsilizila, anakambanso za ena amene adzacilikiza abale a Khiristu ndi kukhala ndi moyo pa dziko lapansi kwamuyaya. (Mat. 25:31-46) Mofananamo, kukwanilitsika koyamba kwa ulosi wa Ezekieli kumakhudza Akhiristu amene ali na ciyembekezo copita kumwamba. Koma ngakhale kuti mafuko 10 a Isiraeli saimila anthu amene adzakhala pa dziko, mgwilizano umene unafotokozedwa mu ulosiwu umatikumbutsa za mgwilizano umene ulipo pakati pa anthu amenewa ndi amene ali na ciyembekezo copita kumwamba.