Mawu Amunsi
c Abale othaŵa kwawo akangofika, akulu ayenela kutsatila malangizo a m’buku la Gulu Lochita Chifunilo ca Yehova mutu 8, palagilafu 30. Akulu angakambilane ndi mipingo ya m’dziko limene kunacokela abalewo mwa kulemba kalata ndi kuitumiza ku ofesi ya nthambi ya m’dziko lawo kupitila pa jw.org. Poyembekezela, iwo mosamala angafunse abale othaŵa kwawo za mipingo imene anali kusonkhanako, ndi zokhudza utumiki kuti adziŵe umoyo wawo wauzimu.