Mawu Amunsi
a Yesu sanaonetse kuti zimene anthu ananenela mtumikiyu zinali zoona kapena zabodza. Liu la Cigiriki limene linamasulidwa kuti “anamuneneza,” pa Luka 16:1, lingatanthauze kuti mtumikiyu anamunamizila. Koma Yesu anasumika maganizo ake pa zimene mtumikiyu anacita, osati pa mlandu umene anafuna kum’cotsela nchito.