Mawu Amunsi
a Anthu ambili sadziŵa kuti mau opezeka m’ma Baibo ena pa Yohane 7:53, Yohane 8:11 ni owonjezela cabe, ndipo sali mbali ya Mau a Mulungu ouzilidwa. Cifukwa ca mau a pa lembali, anthu ena amakamba kuti popeza tonse ndise ocimwa, sitiyenela kumuimba mlandu munthu akacita cigololo. Koma Mulungu anapatsa mtundu wa Aisiraeli lamulo lakuti: “Mwamuna akapezeka akugona ndi mkazi wa mwiniwake, mwamuna ndi mkaziyo, onsewo azifela pamodzi.”—Deut. 22:22.