Mawu Amunsi
b Pa nkhani imeneyi, pulofesa John A. Beck anati: “Malinga n’zimene Ayuda amakhulupilila, Aisiraeli opanduka anamutsutsa Mose na kukamba kuti: ‘Mose wamenya thanthwe ili cifukwa adziŵa kuti n’lofooka. Ngati afuna kuti tikhulupilile kuti alidi na mphamvu yocita zozizwitsa, atitulutsile madzi m’thanthwe lina ili.’” Izi n’zimene Ayuda akhala akukhulupilila, koma zilibe umboni.