Mawu Amunsi
b N’zoonekelatu kuti pa anthu amene adzapulumuka Aramagedo, ena adzakhala olemala. Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, anacilitsa anthu okhala na “zofooka zilizonse.” Izi zinacitila cithunzi zimene iye adzacita kwa opulumuka Aramagedo, osati kwa oukitsidwa. (Mat. 9:35) Mwacidziŵikile, akufa adzaukitsidwa ali na mathupi athanzi, opanda cilema ciliconse.