Mawu Amunsi
a Akatswili ofukula zinthu zakale anapeza zakudya zambili m’matongwe a ku Yeriko. Izi zigwilizana na zimene Baibo imakamba, zakuti Aisiraeli sanazinge mzinda wa Yeriko kwa nthawi yaitali. Olo kuti Aisiraeli sanaloledwe kudya zakudya za mu mzindawo, imeneyi inali nthawi yoyenelela yakuti iwo alande dziko la Kanani cifukwa inali nyengo yokolola, ndipo m’minda munali zakudya zambili.—Yos. 5:10-12.