Mawu Amunsi
a Kukamba zoona, ngakhale anthu amene amakanitsitsa kutengela nzelu za ena, sangapeweletu kusonkhezeledwa na maganizo a anthu ena. Kaya ni poganizila nkhani yaikulu monga ya ciyambi ca moyo, kapena pa nkhani yaing’ono monga ya kusankha covala cakuti avale, munthu aliyense amasonkhezeledwako ndithu na maganizo a ena. Komabe, tili na ufulu wosankha kuti tidzatengela maganizo a ndani.