Mawu Amunsi
a M’lemba la caka ca 2019, muli mfundo zitatu zimene zingatithandize kukhalabe odekha pamene zinthu zoipa zikucitika m’dziko, kapena pamene takumana na mavuto. M’nkhani ino, tidzakambilana mfundo zimenezo. Kucita izi kudzatithandiza kuti tisamakhale na nkhawa kwambili, koma kuti tizidalila Yehova. Muzisinkha-sinkha lemba la caka limeneli. Liloŵezeni pa mtima ngati n’kotheka. Mukatelo, lidzakuthandizani kupilila mavuto amene mudzakumana nawo kutsogolo.