Mawu Amunsi
d MAWU AMUNSI: Mawu akuti “Usacite mantha” amachulidwa maulendo atatu pa Yesaya 41:10, 13, 14. Mavesi amenewa amachulanso mobweleza-bweleza mawu akuti ‘ine’ (kutanthauza Yehova). N’cifukwa ciani Yehova anauzila Yesaya kulemba mobweleza-bweleza mawu akuti ‘ine’? Cifukwa anafuna kugogomeza mfundo yofunika yakuti tingacepetse mantha kokha ngati tidalila Yehova.