Mawu Amunsi
a Mofanana na wamasalimo Davide, tonse timakonda Yehova komanso timafunitsitsa kum’tamanda. Pamene tasonkhana na Akhristu anzathu, timakhala na mwayi wapadela woonetsa kuti timakonda Mulungu. Komabe, ena a ife zimativuta kupeleka ndemanga pamisonkhano. Ngati mumayopa kupeleka ndemanga pa misonkhano, nkhani ino idzakuthandizani kudziŵa zimene zimakupangitsani kuyopa. Komanso idzafotokoza zimene mungacite kuti mucepetse vuto limeneli.