Mawu Amunsi
a Kodi tidzakhalabe okhulupilika kwa Yehova, kapena tidzalola Satana kutikopa mpaka kusiya kutumikila Mulungu? Ngati tiyesetsa kuteteza mtima wathu, tingakhalebe okhulupilika kwa Mulungu, olo titakumana na mayeselo aakulu bwanji. Koma kodi “mtima” umenewu n’ciani? N’ciani cimene Satana amacita pofuna kuipitsa mtima wathu? Nanga tingauteteze bwanji? M’nkhani ino, tidzakambilana mafunso ofunika kwambili amenewa.