Mawu Amunsi
b MAWU OFOTOKOZEDWA: Yehova anatilenga na luso lotha kupenda maganizo na mtima wathu, komanso zocita zathu, kenako n’kudziweluza tekha. M’Baibo, luso limeneli limachedwa cikumbumtima. (Aroma 2:15; 9:1) Cikumbumtima cophunzitsidwa Baibo ni cimene cimaseŵenzetsa mfundo za Yehova, zopezeka m’Mawu ake, potiweluza kuti kaya zoganiza zathu, zocita na zokamba zathu n’zabwino kapena ayi.