Mawu Amunsi
a Posacedwapa, tidzacita mwambo wa Mgonelo wa Ambuye pokumbukila imfa ya Yesu Khristu. Mwambo umenewu umakhala wosacolowana, kapena kuti wosalila zambili. Komabe, mwambowu umatiphunzitsa zambili zokhudza kudzicepetsa kwa Yesu, kulimba mtima, komanso cikondi cake. M’nkhani ino, tidzakambilana zimene tingacite potengela makhalidwe ake amenewa.