Mawu Amunsi
a Cikumbutso ca imfa ya Khristu cimene cidzacitika pa Cisanu madzulo, pa April 19, 2019, cidzakhala cocitika capadela kwambili m’caka cimeneci. Kodi n’ciani cimatisonkhezela kupezeka pa msonkhanowu? Mwacionekele, timapezekapo cifukwa timafuna kukondweletsa Yehova. M’nkhani ino tidzakambilana makhalidwe amene amatisonkhezela kupezeka pa Cikumbutso komanso pa misonkhano ya mlungu na mlungu.