Mawu Amunsi
a Tonsefe sitinabadwe na khalidwe la kufatsa. Timacita kuliphunzila. Cimakhala copepuka kukhala ofatsa ngati ticita zinthu ndi anthu amtendele. Koma ngati ticita zinthu ndi anthu onyada, kukhala ofatsa kungakhale kovuta. M’nkhani ino, tidzakambilana zinthu zina zimene tiyenela kusamala nazo, kuti tikhalebe na khalidwe labwino limeneli la kufatsa.