Mawu Amunsi
b MAWU OFOTOKOZEDWA: Zamizimu ni zikhulupililo komanso zinthu zina zimene anthu amacita mogwilizana na ziŵanda. Zimaphatikizapo cikhulupililo cakuti munthu akafa, mzimu wake umapitiliza kukhala na moyo kwinakwake komanso umakamba ndi anthu amoyo, maka-maka kupitila mwa munthu wolankhula na mizimu. Zamizimu zimaphatikizaponso zinthu monga umfiti na kuwombeza. Komanso zimaphatikizapo kucita zinthu zamatsenga, monga kutembelela ena, kuwalodza kapena kuvumula (kufumbulula) munthu amene walodzedwa. Koma zamizimu siziphatikizapo maseŵela odabwitsa amene ena amacita cifukwa ca luso lawo kuti akondweletse anthu.