Mawu Amunsi
b MAWU OFOTOKOZEDWA: Tikanena kuti kucitila mwana zolaula, titanthauza kuti munthu wamkulu wagwilitsila nchito mwana kukhutilitsa cilakolako cake ca kugonana. Zingaphatikizepo kugona naye, kumugona mkamwa kapena kumbuyo, kum’sisita malisece, maŵele, kapena matako, kapenanso kumucita zinthu zina zosayenela. Nthawi zambili ana amene amacitilidwa zolaula na atsikana, koma palinso anyamata ambili amene amacitilidwa nkhanza zimenezi. Cinanso, ngakhale kuti ambili amene amacitila ana zolaula ni amuna, palinso akazi ena amene amacita zimenezi.