Mawu Amunsi
b MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pamene abale akuyeletsa m’Nyumba ya Ufumu, m’bale Johnson waleka kuseŵenza kuti akambe na m’bale wina komanso mwana wake. Izi zakhumudwitsa Willson, amene akuyeletsa. Mu mtima mwake, iye akuti, ‘Johnson naye wayambanso kuceza pa nchito m’malo moti aziseŵenza.’ Pambuyo pake, Willson akuona Johnson akuthandiza mlongo wacikulile mokoma mtima. Willson wacita cidwi na zimenezi, ndipo wakumbukila mfundo yakuti ni bwino kuyang’ana kwambili pa makhalidwe abwino a m’bale wakeyo.