Mawu Amunsi
a Nthawi zina, abale na alongo amene ali mu utumiki wanthawi zonse wapadela, angafunike kusiya utumiki wawo, kapena angapatsidwe utumiki wina. M’nkhani ino, tikambilane mavuto amene iwo amakumana nawo, na zimene zingawathandize kujaila umoyo watsopano. Tikambilanenso zimene ena angacite kuti awalimbikitse na kuwathandiza, komanso mfundo za m’Baibo zimene zingatithandize tonse pamene zinthu zasintha mu umoyo wathu.