Mawu Amunsi
f Tifunikanso kupewa kuseŵenzetsa malo a zosangalatsa ocilikizidwa na cipembedzo conama, kapena kugwilizana na mabungwe monga ma youth camps, amene ni ogwilizana na cipembedzo conama. Mabungwe amenewo angaphatikizepo la YMCA (Young Men’s Christian Association), komanso la YWCA (Young Women’s Christian Association). Anthu a m’mabungwe amenewa angakambe kuti zocita zawo si zacipembedzo. Koma zoona zake n’zakuti, mabungwewa amalimbikitsa mfundo na zolinga zacipembedzo.