Mawu Amunsi
a Kodi mumafuna kucita zambili potumikila Yehova? Kodi mumakayikila zakuti iye akali kukugwilitsilani nchito? Kapena simuona kufunika kuwonjezela zocita potumikila Yehova? M’nkhani ino, tidzakambilana njila zosiyana-siyana zimene Yehova amalimbitsila zolaka-laka zathu, na kutipatsa mphamvu kuti tikhale ciliconse cimene angafune kuti akwanilitse cifunilo cake.