Mawu Amunsi
d MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI:Pa tsiku la Mwambo Wophimba Macimo, mkulu wa ansembe waciisiraeli anali kuloŵa m’Malo Oyela Koposa atanyamula zofukiza na makala amoto kuti anunkhilitse m’cipindamo na fungo lokoma. Pambuyo pake, anali kuloŵanso m’Malo Oyela Koposa atanyamula magazi a nsembe zophimba macimo.