Mawu Amunsi
a Yehova anapanga makonzedwe apadela akuti Aisiraeli azilengeza ufulu m’dziko lawo. Anakonza zakuti iwo azikondwelela Caka ca Ufulu. Ife Akhristu sitili pansi pa Cilamulo ca Mose. Olo n’telo, kuphunzila za Caka ca Ufulu kungatipindulitse. M’nkhani ino, tidzaphunzila za Caka ca Ufulu cimene Aisiraeli anali kukondwelela. Tidzaona mmene cimatikumbutsila za makonzedwe amene Yehova anapanga n’colinga cakuti tikhale pa ufulu. Tidzaonanso mmene timapindulila na makonzedwe amenewo.