Mawu Amunsi
a Lemba la caka ca 2020 litilimbikitsa kupanga “ophunzila.” Ife tonse atumiki a Yehova tifunika kumvela lamulo limeneli. Kodi tingawathandize bwanji anthu amene timaphunzila nawo Baibo kuti apite patsogolo mpaka kukhala ophunzil a a Khristu? M’nkhani ino, tidzakambilana mmene tingathandizile ophunzila Baibo kukhala pa ubwenzi na Yehova. Tidzakambilananso zimene zingatithandize kudziŵa ngati tifunika kuleka kuphunzila Baibo na munthu kapena ayi.