Mawu Amunsi
b KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Nkhawa imatanthauza kucita mantha kapena kupanikizika maganizo cifukwa ca vuto linalake. Nkhawa ingabwele cifukwa ca mavuto azacuma, matenda, mavuto a m’banja, kapena mavuto ena. Tingakhalenso na nkhawa cifukwa coganizila macimo amene tinacita m’mbuyomu, kapena cifukwa coganiza kuti tidzakumana na mavuto ena ake kutsogolo.