Mawu Amunsi
a Kwa zaka zingapo, atumwi anali na mwayi woceza na Yesu komanso kuseŵenza naye. Ndipo anakhala naye pa ubwenzi wabwino. Yesu amafuna kuti nafenso tikhale mabwenzi ake. Komabe, si copepuka kwa ife kukhala naye pa ubwenzi monga mmene zinalili kwa atumwi. M’nkhani ino, tikambilana zinthu zina zimene zimapangitsa kuti kucita izi kusakhale kopepuka. Tikambilananso zimene tingacite kuti tipange ubwenzi wolimba na iye, komanso kuti tipitilize kukhala mabwenzi ake.