Mawu Amunsi
a Masiku ano, atumiki ambili a Yehova amakumana na mavuto obwela cifukwa ca ukalamba. Ena akudwala matenda ofooketsa thupi. Ndipo tonsefe nthawi zina timakhala olema. Conco, nkhani ya kuthamanga pa mpikisano ingaoneke yovuta kwambili. M’nkhani ino, tikambilana mmene tonsefe tingathamangile mopilila. Tikambilananso zimene tingacite kuti tipambane pa mpikisano wokalandila moyo umene mtumwi Paulo anakamba.