Mawu Amunsi
a Tikukhala m’dziko lolamulidwa na Satana, tate wake wa bodza. Conco zingakhale zovuta kwambili kuyenda m’coonadi. Umu ni mmenenso zinalili kwa Akhristu a m’nthawi ya atumwi. Pofuna kuthandiza Akhristu amenewo na ife masiku ano, Yehova anauzila mtumwi Yohane kulemba makalata atatu. Mfundo za m’makalata amenewa zingatithandize kudziŵa zinthu zimene zingatilepheletse kuyendabe m’coonadi. Komanso zingatithandize kudziŵa zimene tingacite kuti tisagonje ku zinthu zimenezo.