Mawu Amunsi
f MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pamene mlongo wacitsikana ali ku sukulu, akumvela na kuona zinthu zambili zopangitsa munthu kuona ngati khalidwe la mathanyula n’labwino. (M’zikhalidwe zina, mitundu yosiyana-siyana ya pa utawaleza amaiseŵenzetsa monga cizindikilo ca mcitidwe wa mathanyula.) Pambuyo pake, mlongoyo wapatula nthawi yofufuza kuti alimbitse cikhulupililo cake pa zimene Baibo imaphunzitsa. Izi zam’thandiza kupanga cosankha cabwino.