Mawu Amunsi
a Yehova ni Tate wacikondi, wanzelu, komanso woleza mtima. Makhalidwe amenewa amaonekela bwino tikaganizila mmene analengela zinthu zonse, ndiponso lonjezo lake lakuti adzaukitsa akufa. M’nkhani ino, tikambilana ena mwa mafunso amene tingakhale nawo pankhani ya ciukililo. Tikambilananso mmene tingaonetsele kuti timayamikila cikondi ca Yehova, nzelu, na kuleza mtima kwake.