Mawu Amunsi
c MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale akuuza abwana ake ku nchito kuti masiku ena mkati mwa wiki sazikwanitsa kugwila nchito ya ovataimu. Akuwafotokozela kuti pa masiku amenewo amacita zinthu zauzimu madzulo. Komabe, akuwauzanso kuti ngati pa masiku ena papezeka nchito inayake imene iye afunika kuicita mwamsanga, ni wokonzeka kuigwila nchitoyo pa ovataimu.