Mawu Amunsi
c Buku lina limati: “Ophunzila anali kukhala pafupi na mphunzitsi wawo. Ophunzila akhama, anali kukonzekela kuti akaphunzila akakhale aphunzitsi—nchito imene akazi sanali kuloledwa kugwila. . . . Conco amuna ambili aciyuda akanadabwa kuona Mariya atakhala pansi pafupi na Yesu ali na mtima wofuna kuphunzitsidwa na iye.”