Mawu Amunsi
a Kodi mukhala m’dziko limene muli ufulu wolambila Yehova? Ngati n’conco, kodi mukuiseŵenzetsa bwanji nthawi ya mtendele imeneyo? Nkhani ino ikuthandizani kudziŵa mmene mungatsatilile citsanzo ca Mfumu Asa ya Yuda komanso ca Akhristu a m’nthawi ya atumwi. Iwo anaseŵenzetsa mwanzelu nthawi ya mtendele pamene m’dziko lawo munalibe cosokoneza ciliconse.