Mawu Amunsi
a Kuganizila zakumbuyo mu umoyo wathu kulibe vuto. Koma sitifuna kuganizila zakumbuyo mopambanitsa cakuti n’kulephela kuona ubwino wa umoyo wathu palipano, kapena kutiphimba ku madalitso akutsogolo. Nkhani ino ifotokoza misampha itatu imene ingatipangitse kumakhalabe mu umoyo wakumbuyo. Tikambilane mfundo za m’Baibo na zitsanzo za masiku ano zimene zingatithandize kupewa misampha imeneyi.