Mawu Amunsi
a Zioneka kuti mtumwi Yohane ndiye “wophunzila amene Yesu anali kumukonda kwambili.” (Yoh. 21:7) Conco, ngakhale kuti anali mnyamata, ayenela kuti anali na makhalidwe ambili abwino. Patapita zaka, Yehova anamuseŵenzetsa kulemba zambili ponena za khalidwe la cikondi. M’nkhani ino, tione zina mwa zimene Yohane analemba, ndipo tikambilane zimene tingaphunzilepo pa citsanzo cake.