Mawu Amunsi
a Yesu ananena kuti ophunzila ake adzadziŵika na cikondi cimene amaonetsana pakati pawo. Tonsefe timayesetsa kuonetsa cikondi cimeneci. Tiyenela kukulitsa cikondi cathu pa abale athu mwa kuwakonda mmene timakondela anthu a m’banja lathu lakuthupi. Nkhani ino, idzatithandiza kukhala na cikondi ceni-ceni, na kuyesetsa kucionetsa kwa abale na alongo athu a m’cikhulupililo.