Mawu Amunsi
b MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale amumanga ku nyumba kwake. Mkazi wake na mwana wake akuona pamene apolisi akum’tenga kupita naye. Pamene m’baleyo ali kundende, abale na alongo apita ku nyumba kwake kukalambila Yehova pamodzi na mkazi wake na mwana wake. Mayiyo na mwana wake amapempha Yehova kaŵili-kaŵili kuti awapatse mphamvu zowathandiza kupilila ciyeso cawo. Yehova amawapatsa mtendele wa mumtima na kuwathandiza kukhala olimba mtima. Zotulukapo zake n’zakuti cikhulupililo cawo cimalimba, ndipo cimawapangitsa kuti apilile mwacimwemwe.