Mawu Amunsi
a Ngakhale kuti Yesu anali Mphunzitsi waluso kuposa anthu onse amene anakhalako padziko lapansi, anthu ambili m’nthawi yake anam’kana. Cifukwa ciani? M’nkhani ino, tikambilana zifukwa zinayi. Tidzaonanso cifukwa cake ambili masiku ano, amakhumudwa na zimene otsatila oona a Yesu amakamba na kucita. Ndipo cofunika kwambili, tidzaphunzila cifukwa cake tiyenela kukhala na cikhulupililo colimba mwa Yesu kuti tisapunthwe.