Mawu Amunsi
a Cifukwa ca kupanda ungwilo, tingakambe kapena kucita zinthu zimene zingakhumudwitse abale na alongo athu. Kodi zaconco zikacitika timacita ciani? Kodi timayesetsa kukonzanso ubale wathu? Kodi timapepesa mwamsanga? Kapena mumakhala na maganizo akuti ‘ilo ni vuto lawo osati langa?’ Kapena timakhumudwa msanga na zimene ena angakambe kapena kucita? Kodi timadzilungamitsa pa zimene tacita mwa kukamba kuti ndiye mmene tilili, n’cibadwa cathu? Kapena timaona zimene tacita monga cifooko cimene tiyenela kugwililapo nchito?